SHADO ALIMBIKISA ACHINYAMATA KUGWIRA NTCHITO ZACHIFUNDO

OLEMBA: Kassim Kajosolo

Yemwe akufuna kuimba pa undindo wa phungu wa nyumba ya malamulo ku chigawo cha makungwa m’boma la Thyolo, Allie Ratteef Kajosolo wati achinyamata Ali ndi gawo lalikulu posamala madela awo.

Kajosolo, yemwe akuimila chipani cha UDF, anayankhula izi pomwe achinyamata a m’dera la mfumu yaikulu Bvumbwe m’bomali amasamala chipatala cha chaching’ono cha Makungwa.

Iye anati, “achinyamata ali ndi kuthekela kosintha mmene akufunila dela lawo kuti likhale, izi zikuyambila pa kasamalidwe ka malo ngati chipatala ndi zina.”

Iye analimbikisa achinyamatawa kuti apitilize kugwira ntchito zachifundo ndikuika patsogolo kulimbikila mmoyo wawo.

“Achinyamata masiku ano tikumadalila zolandila, sitikumazipeleka, mkofunika kuti tizizipeleka pogwira ntchito kuti dera lathu litha kukhala lozidalila.” Anatero Kajosolo.

Mtsogoleri wa gulu la achinyamata ku dera la makungwa, Lameck Black, anati kugwira ntchito yozipeleka kukonza pa chipatala chinali chinthu chimodzi mwa zinthu zomwe azipanga kupita kusogolo.

“Tikuyamika kuti achinyamata anatuluka kuzagwira ntchito imeneyi, tikufuna achinyamata tikhale okangalika kupanga ntchito zothandiza dela lathu.” Anatero Black.

Iye anathokoza mfumu yaikulu Bvumbwe, yemwe akufuna kuima pa udindo wa phungu ku chipani cha UDF ndi ena omwe athandiza pa ntchitoyi.

Yemwe anaimila mkulu wa pa chipatalapa, a Nellie phiri anayamikila achinyamata a mderali. Iye anapempha achinyamatawa kuti apitilize kugwira ntchitoyi.

Gulu la achinyamata la Makungwa Lili ndi achinyamata ochokera mmidzi yonse mu dela la mfumu yaikulu Bvumbwe, m’boma la Thyolo.